Ruth 2:14 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nthaŵi yakudya Bowazi adauza Rute kuti, “Bwera kuno, udzadyeko buledi ndi kusunsa nthongo yako m'vinyo.” Choncho adakhala pansi pafupi ndi anthu okolola aja, ndipo adampatsa barele wokazinga. Adadya mpaka kukhuta ndipo barele wina adatsalako.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo pa nthawi ya kudya Bowazi ananena naye, Sendera kuno, nudyeko mkate; nusunse nthongo yako m'vinyo wosasayo. Nakhala iye m'mbali mwa ochekawo; ndipo anamtambasulira dzanja kumninkha tirigu wokazinga, nadya iye, nakhuta, nasiyapo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nthawi ya chakudya cha masana Bowazi anati kwa iye, “Bwera kuno, utenge buledi ndi kusunsa nthongo mu vinyo.” Choncho anakhala pansi pafupi ndi okololawo, ndipo Bowazi anamupatsa chakudya ndi nyama yowotcha. Anadya chilichonse amafuna ndipo chakudya china chinatsalako.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo pa nthawi ya kudya Boazi ananena naye, Sendera kuno, nudyeko mkate; nusunse nthongo yako m'vinyo wosasayo. Nakhala iye m'mbali mwa ocekawo; ndipo anamtambasulira dzanja kumninkha tirigu wokazinga, nadya iye, nakhuta, nasiyapo.