Ruth 2:15 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamene adanyamuka mkaziyo kuti akakunkhe, Bowazi adaŵalangiza antchito ake aja kuti, “Muzimulola mkaziyu kuti azikunkha ngakhale pakati pa mitolo, osamchititsa manyazi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ataumirira kukatola khunkha, Bowazi analamulira anyamata ake ndi kuti, Atole khunkha ngakhale pakati pa mitolo, musamchititse manyazi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Atanyamuka kuti azikakunkha, Bowazi analangiza anyamata ake kuti, “Ngakhale mayiyu azikunkha pakati pa mitolo musamuletse ndi kumuchititsa manyazi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ataumirira kukatola khunkha, Boazi analamulira anyamata ace ndi kuti, Atole khunkha ngakhale pakati pa mitolo, musamcititse manyazi.