Ruth 2:18 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adatenga bareleyo kupita naye ku mudzi, nakaonetsa mpongozi wake. Atatero, adatulutsa chakudya chimene chidatsalira atakhuta chija, napatsa mpongozi wakeyo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
nalisenza nalowa kumudzi; ndipo mpongozi wake anaona khunkhalo; Rute natulutsanso nampatsa mkute uja anausiya atakhuta.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anasenza barele uja kupita naye ku mudzi, nakaonetsa apongozi ake. Kenaka anatulutsa chakudya chimene chinatsalira atakhuta chija ndi kupatsa apongozi ake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
nalisenza nalowa kumudzi; ndipo mpongozi wace anaona khunkhalo; Rute naturutsanso nampatsa mkute uja anausiya atakhuta.