Ruth 2:19 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Naomi adamufunsa kuti, “Unakakunkha kuti lero? Unakagwira ntchitoyi m'munda mwa yani? Ngwodala munthu amene anakukomera mtimayo.” Rute adauza mpongozi wake za munthu amene adagwirako ntchito, adati, “Munthuyo dzina lake ndi Bowazi.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mpongozi wake ananena naye, Unakatola kuti khunkha lero? Ndi ntchito udaigwira kuti? Adalitsike iye amene anakusamalira. Ndipo anamfotokozera mpongozi wake munthu amene anakagwirako ntchito, nati, Dzina lake la munthuyo ndinakagwirako ntchito lero ndiye Bowazi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Apongozi akewo anamufunsa kuti, “Kodi lero unakakunkha kuti? Unakagwira kuti ntchitoyi? Adalitsike munthu amene anakukomera mtimayo.” Ndipo Rute anawuza mpongozi wake za munthu amene ku malo ake anakagwirako ntchito. Iye anati, “Munthuyo dzina lake ndi Bowazi.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mpongozi wace ananena naye, Unakatola kuti khunkha lero? ndi nchito udaigwira kuti? Adalitsike iye amene anakusamalira. Ndipo anamfotokozera mpongozi wace munthu amene anakagwirako nchito, nati, Dzina lace la munthuyo ndinakagwirako nchito lero ndiye Boazi.