Ruth 2:20 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Apo Naomi adauza Rute kuti, “Munthu ameneyo amdalitse Chauta, amene amasunga malonjezo ake kwa anthu amoyo, ngakhalenso kwa anthu akufa.” Ndipo adatinso, “Munthuyo ndi mnansi wathu, mmodzi mwa achibale athu, amene ali ndi udindo wotisamala.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nati Naomi kwa mpongozi wake, Yehova amdalitse amene sanaleke kuwachitira zokoma amoyo ndi akufa. Ndipo Naomi ananena naye, Munthuyo ndiye mbale wathu, ndiye mmodzi wa iwo otiombolera cholowa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Naomi anati kwa mpongozi wakeyo, “Munthu ameneyu amudalitse Yehova, amene sanasiye kuchitira chifundo anthu amoyo ndi akufa omwe. Anatinso munthu ameneyu ndi mnansi wapaphata. Ndiye ali ndi udindo wotisamalira.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nati Naomi kwa mpongozi wace, Yehova amdalitse amene sanaleka kuwacitira zokoma amoyo, ndi akufa. Ndipo Naomi ananena baye, Munthuyu ndiye mbale wathu, ndiye mmodzi wa iwo otiombolera colowa.