Ruth 2:21 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Rute Mmowabuyo adati, “Kuwonjezera pamenepo, munthuyo anandiwuza kuti, ‘Uzitsata antchito angaŵa mpaka atamaliza munda wanga kukolola.’ ”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Rute Mmowabu anati, Ananenanso nane ndithu, Uwaumirire anyamata anga, mpaka atatha kucheka zanga zonse za m'minda.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho Rute Mmowabuyo anati, “Iye anandiwuzanso kuti, ‘Uzitsata antchito angawa mpaka atamaliza kukolola munda wonse.’ ”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Rute Mmoabu anati, Ananenanso nane ndithu, Uwaumirire anyamata anga, mpaka atatha kuceka zanga zonse za m'minda.