Ruth 2:23 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Motero Rute ankatsatira adzakazi a Bowaziwo, namakunkha, mpaka anthu atamaliza kudula barele ndi tirigu. Monsemo Rute ankakhala ndi mpongozi wakeyo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Momwemo anaumirira adzakazi a Bowazi kuti atole khunkha kufikira atatha kucheka barele ndi tirigu; ndipo anakhala iye kwao kwa mpongozi wake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho Rute ankatsatira adzakazi a Bowazi namakunkha mpaka anthu atamaliza kudula barele ndi tirigu. Ndipo amakhalabe ndi mpongozi wakeyo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Momwemo anaumirira adzakazi a Boazi kuti atole khunkha kufikira atatha kuceka barele ndi tirigu; ndipo anakhala iye kwao kwa mpongozi wace.