Ruth 2:3 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Choncho Rute adanyamuka napita kukakunkha ku minda, anthu atakolola kale. Kudangochitika kuti adakafika ku munda wa Bowazi amene anali wa m'banja la Elimeleki.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Namuka iye, nakatola khunkha m'munda namatsata ochekawo; ndipo kudangotero naye kuti deralo la munda linali la Bowazi, ndiye wa banja la Elimeleki.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho Rute ananyamuka kupita kukakunkha ku minda yokololedwa kale. Tsono zinangochitika kuti Rute anafika mʼmunda wa Bowazi, yemwe anali wochokera ku banja la Elimeleki.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Namuka iye, nakatola khunkha m'munda namatsata ocekawo; ndipo kudangotero naye kuti deralo la munda linali la Boazi, ndiye wa banja la Elimeleki.