Ruth 2:9 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Uziyang'ana munda akukololawu, ndipo uziŵatsata pambuyo. Ndaŵauza anyamatawo kuti asakuvute. Tsono ukamamva ludzu, uzipita ku mitsuko ndi kukamwa madzi amene anyamatawo atunga.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Maso ako akhale pa munda achekawo, ndi kuwatsata; kodi sindinawauza anyamata asakukhudze? Ndipo ukamva ludzu, muka kumitsuko, ukamweko otunga anyamatawo,
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Uziyangʼana munda akukolola anyamatawo akamakolola mʼmundamu, ndipo iwe uzitsata pambuyo pawo. Ndawawuza anyamatawo kuti asakuvutitse. Ndipo ukamva ludzu, uzipita ku mitsuko ndi kukamwa madzi amene anyamatawa atunga.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Maso ako akhale pa munda acekawo, ndi kuwatsata; kodi sindinawauza anyamata asakukhudze? Ndipo ukamva ludzu, muka kumitsuko, ukamweko otunga anyamatawo,