Ruth 3:10 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Apo Bowazi adati, “Chauta akudalitse, mwana wanga. Zabwino wachita potsirizazi zikupambana zoyamba zija zimene udachitira mpongozi wako, poti sudapite kwa anyamata osauka kapena olemera.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nati iye, Yehova akudalitse, mwana wanga. Chokoma chako wachichita potsiriza pano, chiposa chakuyamba chija, popeza sunatsata anyamata, angakhale osauka angakhale achuma.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo Bowazi anati, “Mwana wanga, Yehova akudalitse popeza kukoma mtima kumene wasonyeza panoku kwaposa koyamba kaja. Iwe sunathamangire anyamata olemera kapena osauka.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nati iye, Yehova akudalitse, mwana wanga. Cokoma cako wacicita potsiriza pano, ciposa cakuyamba cija, popeza sunatsata anyamata, angakhale osauka angakhale acuma.