Ruth 3:13 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Gona konkuno usiku uno mpaka m'maŵa. Ngati iyeyo adzakuloŵe chokolo, chabwino aloŵe. Koma ngati safuna, ndidzakuloŵa ndine, ndikulumbira pamaso pa Chauta wamoyo. Gona mpaka m'maŵa.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Gona usiku uno, ndipo kudzali m'mawa, akakuombolera, chabwino, akuombolere; koma ngati safuna kukuombolera, pali Yehova, ndidzakuombolera cholowa ndine; gona mpaka m'mawa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Gona konkuno usiku uno mpaka mmawa. Tsono ngati iyeyu adzakulowa chokolo, chabwino alowe. Koma ngati safuna kutero, ine ndikulumbira pamaso pa Yehova Wamoyo kuti ndidzakulowa chokolo. Ugone kuno mpaka mmawa.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Gona usiku uno, ndipo kudzali m'mawa, akakuombolera, cabwino, akuombolere; koma ngati safuna kukuombolera, pali Yehova, ndidzakuombolera colowa ndine; gona mpaka m'mawa.