Ruth 3:14 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Choncho Rute adagona ku mapazi a Bowazi mpaka m'maŵa, koma adadzuka kudakali kamdimabe, chifukwa Bowaziyo sankafuna kuti anthu adziŵe kuti mkaziyo adaabwera kopunthira bareleko.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nagona ku mapazi ake mpaka m'mawa; nalawira asanazindikirane anthu. Pakuti anati, Chisadziwike kuti mkaziyo anadza popunthirapo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho Rute anagona ku mapazi ake mpaka mmawa, koma anadzuka mmamawa kusanayere chifukwa Bowazi anati, “Aliyense asadziwe kuti kopondera barele kunabwera mkazi.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nagona ku mapazi ace mpaka m'mawa; nalawira asanazindikirane anthu, Pakuti anati, Cisadziwike kuti mkaziyo anadza popunthirapo,