Ruth 3:18 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Apongozi akewo adayankha kuti, “Dikira mwana wanga, tiwone m'mene zikhalire zinthu, chifukwa munthuyo salekera pomwepo, koma azikonza zimenezi lero.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anati, Khala ulipo, mwana wanga, mpaka udziwa umo ukhalire mlandu; pakuti munthuyo sadzauleka mpaka atautha mlanduwo lero lino.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka Naomi anati, “Mwana wanga, dikira mpaka titaona mmene zinthu zikhalire chifukwa munthuyu salekera pomwepo, mpaka zinthuzi zitakonzeka lero.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anati, Khala ulipo, mwana wanga; mpaka udziwa umo ukhalire mlandu; pakuti munthuyo sadzauleka mpaka atautha mlanduwo lero lino.