Ruth 3:7 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Bowazi atamaliza kudya ndi kumwa, anali wosangalala, ndipo adapita kukagona pambali pa mulu wa barele. Tsono Rute adabwera mopanda mtswatswa, adavundukula mapazi a Bowazi, nagona pomwepo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo atatha Bowazi kudya ndi kumwa, nusekerera mtima wake, anakagona kuthungo kwa mulu wa tirigu; nadza iye kachetechete, navundukula ku mapazi ake, nagona.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Atamaliza kudya ndi kumwa, Bowazi anakhala wosangalala, ndipo anakagona pa mbali pa mulu wa barele. Tsono Rute anapita mwa kachetechete, navundukula chofunda ku mapazi ake ndi kugona.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo atatha Boazi kudya ndi kumwa, nusekerera mtima wace, anakagona kuthungo kwa mulu wa tirigu; nadza iye kacetecete, nabvuodukula ku mapazi ace, nagona.