Ruth 4:1 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nthaŵi yomweyo Bowazi adapita ku chipata cha mzinda nakakhala pansi, pa bwalo losonkhanirana. Tsono adangoona wachibale ankanena uja akufika. Apo Bowazi adati, “Bwenzi langa, tapatukira kuno, ukhale pansi apa.” Munthu uja adapatuka nakhala pansi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Bowazi anakwera kunka kuchipata, nakhala pansi pomwepo; ndipo taona, woombolera winayo adanena Bowazi analinkupita; nati iye, Iwe uje, patuka, khala pansi apa; napatuka iye, nakhala pansi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nthawi yomweyo Bowazi anapita ku chipata cha mzinda ndi kukhala pansi kumeneko pabwalo losonkhanira. Tsono anangoona wachibale woyenera kulowa chokolo uja akufika. Ndipo Bowazi anati, “Patukirani kuno, bwenzi langa. Mubwere mudzakhale apa.” Choncho anapatuka nakakhala pansi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Boazi anakwera kumka kucipata, nakhala pansi pomwepo; ndipo taona, woombolera winayo adanena Boazi analinkupita; nati iye, Iwe uje, pambuka, khala pansi apa; napambuka iye, nakhala pansi.