Ruth 4:11 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Apo anthu onse amene anali pachipata paja, pamodzi ndi atsogoleri aja, adati, “Inde, ndife mboni. Mkazi amene akudzaloŵa m'nyumba mwakoyo, Chauta amsandutse wofanafana ndi Rakele ndi Leya, akazi amene adamanga banja la Israele pombalira ana ambiri. Ukhale munthu wosasoŵa kanthu mu mzinda wa Efurata, ndipo ukhale munthu wotchuka mu mzinda wa Betelehemu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo anthu onse anali kuchipata, ndi akulu, anati, Tili mboni ife. Yehova achite kuti mkazi wakulowayo m'nyumba mwako ange Rakele ndi Leya, amene anamanga nyumba ya Israele, iwo awiri; nuchite iwe moyenera m'Efurata, numveke m'Betelehemu;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo akuluakulu aja ndi anthu onse amene anali pa chipata anati, “Ife ndife mboni, ndipo Yehova amusandutsa mkazi amene akudzalowa mʼnyumba yakoyu kuti akhale ngati Rakele ndi Leya, amene anamanga banja la Israeli. Ukhale munthu wosasowa kanthu mu Efurata ndi munthu wotchuka mu Betelehemu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo anthu onse anali kucipata, ndi akuru, anati, Tiri mboni ife. Yehova acite kuti mkazi wakulowayo m'nyumba mwako ange Rakele ndi Leya, amene anamanga nyumba ya Israyeli, iwo awiri; nucite iwe moyenera m'Efrata, numveke m'Betelehemu;