Ruth 4:13 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Choncho Bowazi adakwatira Rute, ndipo Chauta adadalitsa Ruteyo, mwakuti adatenga pathupi nabala mwana wamwamuna.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Momwemo Bowazi anatenga Rute, nakhala iye mkazi wake; ndipo analowa kwa iye; nalola Yehova kuti aime, ndipo anabala mwana wamwamuna.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho Bowazi anakwatira Rute. Yehova anamudalitsa nakhala ndi pakati, ndipo anabereka mwana wamwamuna.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Momwemo Boazi anatenga Rute, nakhala iye mkazi wace; ndipo analowa kwa iye; nalola Yehova kuti aime, ndipo anabala mwana wamwamuna.