Ruth 4:15 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mwanayo adzakupatsani moyo watsopano ndipo adzakuchirikizani mu ukalamba wanu. Inde wakubalirani mwana mpongozi wanu amene amakukondani, amene wakuwonetsani kuti akupambana ana aamuna asanu ndi aŵiri.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nakhale uyu wakukubwezera moyo, ndi wodyetsa ukalamba wako; pakuti mpongozi wako amene akukonda, amene aposa ana amuna asanu ndi awiri kukuthandiza, anambala.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mwanayo adzakupatseni moyo watsopano ndi kukuthandizani pa ukalamba wanu. Inde, mpongozi wanu amene amakukondani, amenenso waonetsa kuti ali wopambana kwa inu kuposa ana aamuna asanu ndi awiri, ndiye wakubalirani mwanayu.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nakhale uyu wakukubwezera moyo, ndi wodyetsa ukalamba wako; pakuti mpongozi wako amene akukonda, amene aposa ana amuna asanu ndi awiri kukuthandiza, anambala.