Ruth 4:3 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono adauza munthu wachibale uja kuti, “Naomi amene wabwerera kuchokera ku dziko la Mowabu, akugulitsa munda umene udaali wa malemu Elimeleki, wachibale wathu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo anati kwa woombolerayo, Naomi anabwerayo ku dziko la Mowabu ati agulitse kadziko kaja kadali ka mbale wathu Elimeleki;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka anamuwuza oyenera kulowa chokolo uja kuti, “Naomi amene wabwera kuchoka ku Mowabu akugulitsa malo amene anali a malemu Elimeleki, mʼbale wathu uja.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo anati kwa woombolerayo, Naomi anabwerayo ku dziko la Moabu ati agulitse kadziko kala kadali ka mbale wathu Elimeleki;