Ruth 4:5 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Bowazi adamuuza kuti, “Tsiku limene udzagule mundawo kwa Naomi, udzatenganso Rute Mmowabu, mai wamasiye uja, kuti dzina la malemu aja lisungike pa choloŵa chao.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nati Bowazi, Tsiku lomwelo ugula mundawo pa dzanja la Naomi, uugulanso kwa Rute, Mmowabu, mkazi wa wakufayo, kuukitsira dzina la wakufayo pa cholowa chake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono Bowazi anati, “Tsiku limene ukagule mundawo kwa Naomi, udzatenganso Rute Mmowabu, mkazi wamasiye uja, kuti dzina la malemu lisungike pa cholowa chake.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nati Boazi, Tsiku lomwelo ugula mundawo pa dzanja la Naomi, uugulanso kwa Rute, Mmoabu, mkazi wa wakufayo, kuukitsira dzina la wakufayo pa colowa cace.