Ruth 4:7 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Masiku amenewo, munthu akamachita malonda kapena kusinthana kanthu ndi mnzake, zinkayenda motere: ankavula nsapato imodzi napatsa mnzakeyo. Imeneyi ndiyo inali njira yochitira umboni m'dziko la Israele.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma kale m'Israele pakuombola ndi pakusinthana, kutsimikiza mlandu wonse, akatero: munthu avula nsapato yake, naipereka kwa mnansi wake; ndiwo matsimikizidwe m'Israele.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
(Kale mu Israeli zinkatere ngati munthu afuna kuwombola kanthu kapena kusinthana kanthu ndi mnzake kuti chikhale chakechake. Iye ankavula nsapato imodzi namupatsa mnzakeyo. Imeneyo ndiyo inali njira yochitira umboni mu Israeli).
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma kale m'Israyeli pakuombola ndi pakusinthana, kutsimikiza mlandu wonse, akatero: munthu abvula nsapato yace, naipereka kwa mnansi wace; ndiwo matsimikizidwe m'Israyeli.
Recommended Reading