Ruth 4:9 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Bowazi adauza atsogoleri ndi anthu onse aja kuti, “Nonsenu ndinu mboni lero, kuti ine ndagula kwa Naomi zonse zimene zidaali za malemu Elimeleki, ndiponso zonse za malemu Kiliyoni ndi za malemu Maloni.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nati Bowazi kwa akulu, ndi kwa anthu onse, Inu ndinu mboni lero lino kuti ndagula zonse za Elimeleki, ndi zonse za Kilioni, ndi Maloni, pa dzanja la Naomi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo Bowazi anawuza akuluakuluwo ndi anthu onse aja kuti, “Nonsenu ndinu mboni lero, kuti ine ndagula kwa Naomi zonse zimene zinali za malemu Elimeleki, zonse zimene zinali za malemu Kiliyoni ndiponso za malemu Maloni.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nati Boazi kwa akulu, ndi kwa anthu onse, Inu ndinu mboni lero lino kuti ndagula zonse za Elimeleki, ndi zonse za Kilioni, ndi Maloni, pa dzanja la Naomi.