Song of Solomon 1:6 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Musandiyang'ane monyoza chifukwa cha kudaku, ndi dzuŵatu lidandidetsali. Alongo anga adandikwiyira, mpaka kukandigwiritsa ntchito m'minda yamphesa. Koma munda wangawanga, osatha kuusamala.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Musayang'ane pa ine, pakuti ndada, pakuti dzuwa landidetsa. Ana amuna a amai anandikwiyira, anandisungitsa minda yamipesa; koma munda wangawanga wamipesa sindinausunga.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Musandiyangʼane monyoza chifukwa ndine wakuda, ndine wakuda chifukwa cha dzuwa. Alongo anga anandikwiyira ndipo anandigwiritsa ntchito mʼminda ya mpesa; munda wangawanga sindinawusamalire.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Musayang'ane pa ine, pakuti ndada, Pakuti dzuwa landidetsa. Ana amuna a amai anandikwiyira, Anandisungitsa minda yamipesa; Koma munda wanga wanga wamipesa sindinausunga.