Song of Solomon 1:8 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Iwe wokongola koposa akazi onsewe, ngati sukukudziŵa, uzingotsata m'makwalala a msambi wa ziŵeto, uzidyetsa mbuzi zako pambali pa mahema a abusawo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ngati sudziwa, mkaziwe woposa kukongola, dzituluka kukalondola bande la gululo, nukawete anaambuzi zako pambali pa mahema a abusa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ngati sukudziwa iwe wokongola kwambiri kuposa akazi ena, ngati sukudziwa, tsatira makwalala a nkhosa ndipo udyetse ana ambuzi pambali pa matenti a abusa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ngati sudziwa, mkaziwe woposa kukongola, Dzituruka kukalondola bande la gululo, Nukawete ana a mbuzi zako pambali pa mahema a abusa.