Song of Solomon 2:12 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Maluŵa ayamba kuwoneka m'dziko, nthaŵi yoimba yafika, njiŵa zikumveka kulira m'dziko mwathu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
maluwa aoneka pansi; nthawi yoimba mbalame yafika, mau a njiwa namveka m'dziko lathu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Maluwa ayamba kuoneka pa dziko lapansi; nthawi yoyimba yafika, kulira kwa njiwa kukumveka mʼdziko lathu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Maluwa aoneka pansi; Nthawi yoyimba mbalame yafika, Mau a njiwa namveka m'dziko lathu;