Song of Solomon 2:17 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kamphepo kamadzulo kakamayamba kuuzira, mithunzi ikamayamba kuthaŵa, unyamuke, iwe wokondedwa wanga, uthamange ngati mphoyo, kapena ngati mwanawambaŵala pakati pa mapiri azigwembezigwembe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mpaka dzuwa litapepa, mithunzi ndi kutanimpha, bwera, bwenzi langawe, nukhale ngati mphoyo pena mwana wa mbawala pa mapiri a mipata.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kamphepo kamadzulo kakayamba kuwuzira ndipo mithunzi ikayamba kuthawa, unyamuke bwenzi langa, ndipo ukhale ngati gwape kapena ngati mwana wa mbawala pakati pa mapiri azigwembezigwembe.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mpaka dzuwa litapepa, mithunzi ndi kutanimpha, Bwera, bwenzi langawe, nukhale ngati mphoyo pena mwana wa mbawala Pa mapiri a mipata.