Song of Solomon 2:3 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Muja umakhalira mtengo wa apulosi pakati pa mitengo yam'nkhalango, ndi m'mene aliri wokondedwa wanga pakati pa anyamata. Ndinkakondwa kwambiri ndikausa mumthunzi mwake, zipatso zake zinali tseketseketseke m'kamwamu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ngati maula pakati pa mitengo ya m'nkhalango, momwemo wokondedwa wanga pakati pa ana amuna. Ndinakondwa pakukhala pa mthunzi wake, zipatso zake zinatsekemera m'kamwa mwanga.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Monga mtengo wa apulosi pakati pa mitengo ya mʼnkhalango ndi momwe alili bwenzi langa pakati pa anyamata. Ndimakondwera kukhala pansi pa mthunzi wako, ndipo chipatso chake ndi chokoma mʼkamwa mwanga.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ngati maula pakati pa mitengo ya m'nkhalango, Momwemo wokondedwa wanga pakati pa ana amuna. Ndinakondwa pakukhala pa mthunzi wace, Zipatso zace zinatsekemera m'kamwa mwanga.