Song of Solomon 2:9 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Wokondedwa wanga ali ngati mphoyo, kapena mwanawambaŵala. Si uyo waimirira apoyo, kuseri kwa khoma lathulo, akusuzumira m'mawindo, akuyang'anira pa made a mawindo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Wokondedwa wanga akunga mphoyo, pena mwana wa mbawala: Taona, aima patseri pakhoma lathu. Apenyera pazenera, nasuzumira pamade.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Bwenzi langa ali ngati gwape kapena mwana wa mbawala. Taonani! Uyo wayima kuseri kwa khoma lathulo, akusuzumira mʼmazenera, akuyangʼana pa mpata wa zenera.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Wokondedwa wanga akunga mphoyo, pena mwana wa mbawala: Taona, aima patseri pa khoma pathu, Apenyera pazenera, Nasuzumira pamade.