Song of Solomon 3:11 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tulukani, inu akazi a ku Ziyoni, mudzaone Mfumu Solomoni, atavala chisoti chaufumu chimene mai wake adamuveka pa tsiku la ukwati wake, tsiku limene mtima wake unkasangalala.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Tulukani, ana akazi inu a Ziyoni, mupenye Solomoni mfumu, ndi korona amake amamveka naye tsiku la ukwati wake, ngakhale tsiku lakukondwera mtima wake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tukulani inu akazi a ku Ziyoni ndipo mudzaone mfumu Solomoni atavala chipewa chaufumu, chipewa chaufumu chimene amayi ake anamuveka pa tsiku la ukwati wake, tsiku limene mtima wake unasangalala.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Turukani, ana akazi inu a Ziyoni, mupenye Solomo mfumu, Ndi korona amace anambveka naye tsiku la ukwati wace, Ngakhale tsiku lakukondwera mtima wace.