Song of Solomon 3:4 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndidangoti iwo aja ntaŵapitirira pang'ono, ndampeza amene mtima wanga umamkonda. Ndidamgwira, osamlola kuti achoke, mpaka nditamloŵetsa m'nyumba ya amai anga, m'chipinda cha amene adandibala.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nditawapitirira pang'ono, ndinampeza amene moyo wanga umkonda: Ndinamgwiriziza, osamfumbatula, mpaka nditamlowetsa m'nyumba ya amai, ngakhale m'chipinda cha wondibala.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nditawapitirira pangʼono ndinamupeza amene mtima wanga umamukonda. Ndinamugwira ndipo sindinamulole kuti achoke mpaka nditamulowetsa mʼnyumba ya amayi anga, mʼchipinda cha amene anandibereka.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nditawapitirira pang'ono, Ndinampeza amene moyo wanca umkonda: Ndinamgwiriziza, osamfumbatula, Mpaka nditamlowetsa m'nyumba ya amai, Ngakhale m'cipinda ca wondibala.