Song of Solomon 4:1 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndiwe wokongola, iwe wokondedwa wanga! Ndithuditu, ndiwe wokongoladi! Kumbuyo kwa nsalu yako yakumutuyo maso ako akuwoneka oŵala ngati nkhunda. Tsitsi lako likuchita pekupeku ngati mbuzi zoti zikutsetsereka pa mapiri a ku Giliyadi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Taona, wakongola, bwenzi langa, namwaliwe, taona, wakongola; maso ako akunga a nkhunda patseri pa chophimba chako. Tsitsi lako likunga gulu la mbuzi, zooneka pa phiri la Giliyadi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndiwe wokongoladi wokondedwa wanga! Ndithudi, ndiwe wokongola! Maso ako ali ngati nkhunda kumbuyo kwa nsalu yophimba kumutu. Tsitsi lako lili ngati gulu la mbuzi zikutsetsereka kuchokera ku Giliyadi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Taona, wakongola, bwenzi langa, namwaliwe, taona, wakongola; Maso ako akunga a nkhunda patseri pa cophimba cako: Tsitsi lako likunga gulu la mbuzi, Zooneka pa phiri la Gileadi.