Song of Solomon 4:10 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Iwe mlongo wanga, iwe mkazi wanga, chikondi chako nchosangalatsa. Chikondi chako nchosangalatsa kupambana vinyo, mafuta ako ndi onunkhira bwino kupambana zonunkhira zabwino zonse.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ha, chikondi chako nchokongola, mlongo wanga, mkwatibwi! Kodi chikondi chako sichiposa vinyo? Kununkhira kwa mphoka yako ndi kuposa zonunkhiritsa za mitundumitundu!
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iwe mlongo wanga, mkwatibwi wanga, chikondi chako nʼchosangalatsa! Chikondi chako nʼchosangalatsa kwambiri kupambana vinyo, ndiponso fungo la mafuta ako ndi lopambana zonunkhiritsa zonse!
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ha, cikondi cako ncokongola, mlongwanga, mkwatibwi! Kodi cikondi cako siciposa vinyo? Kununkhira kwa mphoka yako ndi kuposa zonunkhiritsa za mitundu mitundu!