Song of Solomon 4:11 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Iwe mkazi wanga, milomo yako ili uchi mvee! Kunsi kwa lilime lako kuli ngati uchi ndi mkaka. Fungo la zovala zako likumveka ngati fungo la ku Lebanoni.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
M'milomo yako, mkwatibwi, mukukha uchi, uchi ndi mkaka zili pansi pa lilime lako; kununkhira kwa zovala zako ndi kunga kununkhira kwa Lebanoni.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iwe mkwatibwi wanga, milomo yako ikuchucha uchi ngati chisa cha njuchi; pansi pa lilime lako pali mkaka ndi uchi. Fungo lonunkhira la zovala zako likumveka ngati fungo la ku Lebanoni.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
M'milomo yako, mkwatibwi, mukukha uci, Uci ndi mkaka ziri pansi pa lilime lako; Kununkhira kwa zobvala zako ndi kunga kununkhira kwa Lebano,