Song of Solomon 4:16 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Dzuka, iwe mphepo yakumpoto, bwera kuno, iwe mphepo yakumwera. Uuzire pa munda wanga kuti fungo lake lokoma likwanire ponseponse. Wokondedwa wanga aloŵe m'munda mwake, adye zipatso zake zokoma.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Galamuka, mphepo ya kumpoto iwe, nudze, mphepo iwe ya kumwera; nuombe pamunda panga, kuti zonunkhiritsa zake zitulukemo. Bwenzi langa mnyamatayo, alowe m'munda mwake, nadye zipatso zake zofunika.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Dzuka, iwe mphepo yakumpoto, ndipo bwera, iwe mphepo yakummwera! Uzira pa munda wanga, kuti fungo lake lonunkhira lifalikire ponseponse. Bwenzi langa alowe mʼmunda mwake ndi kudya zipatso zake zabwino kwambiri.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Galamuka, mphepo ya kumpoto iwe, nudze, mphepo iwe ya kumwela; Nuombe pamunda panga, kuti zonunkhiritsa zace ziturukemo. Bwenzi langa mnyamatayo, alowe m'munda mwace, Nadye zipatso zace zofunika.