Song of Solomon 4:8 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tiye tichokeko ku Lebanoni, iwe mkazi wanga. Tiye tichoke ku Lebanoni kuno, utsagane ndi ine. Utsikepo pa nsonga ya phiri la Amana, pa nsonga ya phiri la Seniri ndi la Heremoni. Uchokemo m'mapanga a mikango, uchokeko ku ngaka za akambuku.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Idza nane kuchokera ku Lebanoni, mkwatibwi, kuchokera nane ku Lebanoni: Unguza pamwamba pa Amana, pa nsonga ya Seniri ndi Heremoni, pa ngaka za mikango, pa mapiri a anyalugwe.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tiye tichoke ku Lebanoni iwe mkwatibwi wanga, tiye tichoke ku Lebanoni, utsikepo pa msonga ya Amana, kuchoka pa msonga ya phiri la Seniri, pamwamba penipeni pa Herimoni, kuchoka ku mapanga a mikango ndiponso kumapiri kumene akambuku amavutitsa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Idza nane kucokera ku Lebano, mkwatibwi, Kucokera nane ku Lebano: Unguza pamwamba pa Amana, Pa nsonga ya Seniri ndi Hermoni, Pa ngaka za mikango, Pa mapiri a anyalugwe.