Song of Solomon 4:9 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Iwe mlongo wanga, iwe mkazi wanga, wangoti mtima wangawu kwe! Wanditenga mtima ndi kapenyedwe ka maso ako, ndiponso ndi mphande imodzi ya mkanda wa m'khosi mwako.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Walanda mtima wanga, mlongo wanga, mkwatibwi; walanda mtima wanga ndi diso lako limodzi, ndi chinganga chimodzi cha pakhosi pako.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iwe mlongo wanga, mkwatibwi wanga, wanditenga mtima, iwe wanditenga mtima ndi kapenyedwe ka maso ako, ndiponso ndi umodzi mwa mikanda ya mʼkhosi mwako.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Walanda mtima wanga, mlongwanga, mkwatibwi; Walanda mtima wanga ndi diso lako limodzi, Ndi cinganga cimodzi ca pakhosi pako,