Song of Solomon 5:1 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndaloŵa m'munda mwanga, iwe mlongo wanga, iwe mkazi wanga. Ndikukolola mure wanga ndi zokometsera chakudya. Ndikudya uchi wanga pamodzi ndi zisa zake zomwe. Ndikumwa vinyo wanga ndi mkaka wanga. Akazi Inu apaubwenzi, idyani ndi kumwa: Inu okondana, imwani kwambiri! Mkazi
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndalowa m'munda mwanga, mlongo wanga, mkwatibwi: Ndatchera mure wanga ndi zonunkhiritsa zanga; ndadya uchi wanga ndi chisa chake; ndamwa vinyo wanga ndi mkaka wanga. Idyani, atsamwalinu, imwani, mwetsani chikondi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndalowa mʼmunda mwanga, iwe mlongo wanga, iwe mkwatibwi wanga; ndasonkhanitsa mure wanga ndi zokometsera zakudya zanga. Ndadya uchi wanga pamodzi ndi zisa zake zomwe; ndamwa vinyo wanga ndi mkaka wanga. Idyani abwenzi anga, imwani; Inu okondana, imwani kwambiri.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndalowa m'munda mwanga, mlongwanga, mkwatibwi: Ndachera nipa yanga ndi zonunkhiritsa zanga; Ndadya uci wanga ndi cisa cace; Ndamwa vinyo wanga ndi mkaka wanga. Idyani, atsamwalinu, Imwani, mwetsani cikondi.