Song of Solomon 5:11 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mutu wake uli ngati golide wosalala kwambiri. Tsitsi lake nlopotana bwino, lakuda bwino ngati nthenga za khwangwala.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mutu wake ukunga golide, woyengetsa, tsitsi lake lopotana, ndi lakuda ngati khungubwi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mutu wake ndi golide woyengeka bwino; tsitsi lake ndi lopotanapotana, ndiponso lakuda bwino ngati khwangwala.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mutu wace ukunga golidi, woyengetsa, Tsitsi lace lopotana, ndi lakuda ngati khungubwi.