Song of Solomon 5:13 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Masaya ake ali ngati timinda ta mbeu zokometsera chakudya, zopatsa fungo lokoma. Milomo yake ili ngati akakombo, ili noninoni ndi zodzoladzola za mure.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Masaya ake akunga chitipula chobzalamo ndiwo, ngati mitumbira yoyangapo masamba onunkhira: Milomo yake ikunga akakombo, pakukhapo madzi a mure.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Masaya ake ali ngati timinda ta mbewu zokometsera zakudya zopatsa fungo lokoma. Milomo yake ili ngati maluwa okongola amene akuchucha mure.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Masaya ace akunga citipula cabzyalamo ndiwo, Ngati mitumbira yoyangapo masamba onunkhira: Milomo yace ikunga akakombo, pakukhapo madzi a nipa.