Song of Solomon 5:15 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Miyendo yake ili ngati mizati yamwala yokhazikika pa maziko agolide. Ali ndi maonekedwe aulemerero ngati mapiri a ku Lebanoni, maonekedwe aulemu ngati mitengo ya paini ya pamapiripo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Miyendo yake ikunga zoimiritsa za mwala wonyezimira, zogwirika m'kamwa mwa golide: Maonekedwe ake akunga Lebanoni, okometsetsa ngati mikungudza.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Miyendo yake ili ngati mizati yamwala, yokhazikika pa maziko a golide. Maonekedwe ake ali ngati Lebanoni, abwino kwambiri ngati mkungudza.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Miyendo yace ikunga zoimiritsa za mwala wonyezimira, Zogwirika m'kamwa mwa golidi: Maonekedwe ace akunga Lebano, okometsetsa ngati mikungudza.