Song of Solomon 5:2 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kugona ndinagona, koma mtima wanga unali maso. Tamverani! Wokondedwa wanga akugogoda. Mwamuna “Tanditsekulira iwe mlongo wanga, iwe wokondedwa wanga, iwe nkhunda yanga, iwe wangwiro wanga. Mutu wanga wanyowa ndi mame, tsitsi langa lachita madzi chifukwa cha nkhungu yausiku.” Mkazi
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndinagona tulo, koma mtima wanga unali maso: Ndi mau a bwenzi langa mnyamatayo agogoda, nati, nditsegulire, mlongo wanga, wokondedwa wanga, nkhunda yanga, wangwiro wanga: Pakuti pamtu panga padzala mame, patsitsi panga pali madontho a usiku.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndinagona tulo koma mtima wanga unali maso. Tamverani, bwenzi langa akugogoda: “Nditsekulire, mlongo wanga, bwenzi langa, nkhunda yanga, wangwiro wanga. Mutu wanga wanyowa ndi mame, tsitsi langa lanyowa chifukwa cha nkhungu ya usiku.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndinagona tulo, koma mtima wanga unali maso: Ndi mau a bwenzi langa mnyamatayo agogoda, nati, Nditsegulire, mlongwanga, wokondedwa wanga, nkhunda yanga, wangwiro wanga: Pakuti pamtu panga padzala mame, Patsitsi panga pali madontho a usiku.