Song of Solomon 5:6 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndidamtsekulira wokondedwa wanga, koma nkuti iyeyo atachokapo, atapita. Pamene iye ankalankhula, mtima wanga udangoti fumu! Ndidamfunafuna koma osampeza. Ndidamuitana, koma iye osandiyankha.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndinamtsegulira bwenzi langalo; koma ndinampeza, bwenzi langa atachoka. Moyo wanga unalefuka polankhula iye: Ndinamfunafuna, osampeza; ndinamuitana, koma sanandivomere.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndinamutsekulira wachikondi wanga, koma nʼkuti wachikondi wangayo atachoka; iye anali atapita. Mtima wanga unafumuka chifukwa cha kuchoka kwake. Ndinamuyangʼanayangʼana koma sindinamupeze. Ndinamuyitana koma sanandiyankhe.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndinamtsegulira bwenzi langalo; Koma ndinampeza, bwenzi langa atacoka. Moyo wanga unalefuka polankhula iye: Ndinamfunafuna, osampeza; Ndinamuitana, koma sanandibvomera.