Song of Solomon 6:11 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndidatsikira ku munda wa mitengo ya alimondi, kuti ndikayang'ane maluŵa akuchigwa, kuti ndikaone ngati mipesa idaphukira, ngati makangaza adachita maluŵa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndinatsikira kumunda wa mtedza, kukapenya msipu wa m'chigwa, kukapenya ngati pamipesa paphuka, ngati pamakangaza patuwa maluwa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndinatsikira ku munda wa mitengo ya alimondi kukayangʼana zomera zatsopano ku chigwa, kukaona ngati mpesa waphukira kapena ngati makangadza ali ndi maluwa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndinatsikira ku munda wa ntedza, Kukapenya msipu wa m'cigwa, Kukapenya ngati pamipesa paphuka, Ngati pamakangaza patuwa maluwa.