Song of Solomon 6:9 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma ine nkhunda yanga, wangwiro wanga, ndi mmodzi yekha basi, mwana mmodzi yekha wa amai ake, mwana wapamtima wa amai ake. Anamwali atamuwona, adamutcha wodala. Akazi enieni a mfumu ndi akazi onse aang'ono adamtamanda.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nkhunda yanga, wangwiro wangayu, ndiye mmodzi; ndiye wobadwa yekha wa amake; ndiye wosankhika wa wombala. Ana akazi anamuona, namutcha wodala; ngakhale akazi akulu a mfumu, ndi akazi aang'ono namtamanda.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
koma nkhunda yanga, wangwiro wanga ndi wosiyana ndi wina aliyense; mwana wamkazi yekhayo wa amayi ake, mwana wapamtima wa amene anamubereka. Anamwali anamuona ndipo anamutcha wodala; akazi a mfumu ndi azikazi anamutamanda.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nkhunda yanga, wangwiro wangayu, ndiye mmodzi; Ndiye wobadwa yekha wa amace; Ndiye wosankhika wa wombala. Ana akazi anamuona, namucha wodala; Ngakhale akazi akulu a mfumu, ndi akazi ang'ono namtamanda.