Song of Solomon 7:1 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Iwe namwali wachifumu, mapazi ako ngokongola m'nsapato wavalazo. Ntchafu zako nzoulungika bwino ngati miyala yamtengowapatali, yosemedwa ndi mmisiri waluso.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ha, mapazi ako akongola m'zikwakwata, mwana wamkaziwe wa mfumu! Pozinga m'chuuno mwako pakunga zonyezimira, ntchito ya manja a mmisiri waluso.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iwe namwali waufumu, mapazi ako ngokongola mu nsapato wavalazo! Ntchafu zako nʼzowumbika bwino ngati miyala yamtengowapatali, ntchito ya manja ya mmisiri waluso.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ha, mapazi ako akongola m'zikwakwata, Mwana wamkaziwe wa mfumu! Pozinga m'cuuno mwako pakunga zonyezimira, Nchito ya manja a mmisiri waluso.