Song of Solomon 7:12 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tiye tilaŵirire m'mamaŵa kupita ku minda yamphesa, tikaone ngati mipesa idaphuka, ngati nkhunje zake zidachita maluŵa, ndiponso ngati makangaza adachita maluŵa. Kumeneko ndidzakuwonetsa chikondi changa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Tilawire kunka kuminda yamipesa; tiyang'ane ngati mpesa waphuka, kunje ndi kuonetsa zipatso, makangaza ndi kutuwa maluwa ake; pompo ndidzakupatsa chikondi changa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tiye tilawirire mmamawa kupita ku minda ya mpesa, tikaone ngati mitengo ya mpesa yayamba kuphukira, ngati maluwa ake ayamba kuoneka, komanso ngati makangadza ayamba kuonetsa maluwa. Kumeneko ndidzakuonetsa chikondi changa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Tilawire kunka ku minda yamipesa; Tiyang'ane ngati mpesa waphuka, kunje ndi kuonetsa zipatso, Makangaza ndi kutuwa maluwa ace; Pompo ndidzakupatsa cikondi canga,