Song of Solomon 7:5 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mutu wako uli bwinobwino neng'a, ngati phiri la Karimele, ndipo tsitsi lako lalitali lili chezichezi. Kukongola kwake kumatha kudolola ndi mfumu yomwe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mutu wako ukunga Karimele, ndi tsitsi la pamtu pako likunga nsalu yofiirira; mfumu yamangidwa ndi nkhata zake ngati wam'nsinga.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mutu wako uli bwinobwino nengʼaa ngati phiri la Karimeli. Tsitsi lako lili ngati nsalu yakuda yaufumu; mfumu yakopeka ndi maonekedwe ake okongola.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mutu wako ukunga Karimeli, Ndi tsitsi la pamtu pako likunga nsaru yakuda; Mfumu yamangidwa ndi nkhata zace ngati wamsinga.