Song of Solomon 7:8 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndidati, ndikwera mu mtengo wa mgwalangwawu, ndikathyole zipatso zake. Maŵere ako akhale ngati masango a mphesa, fungo la mpweya wako likhale lonunkhira bwino ngati la maapulosi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndinati, Ndikakwera pa mgwalangwapo, ndikagwira nthambi zake: Mawere ako ange ngati matsango amphesa, ndi kununkhira kwa mpweya wako ngati maula.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndinati, “Ndikwera mtengo wa mgwalangwa; ndidzathyola zipatso zake.” Mawere ako ali ngati maphava a mphesa, fungo la mpweya wako lili ngati ma apulosi,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndinati, Ndikakwera pamlazapo, Ndikagwira nthambi zace: Maere ako ange ngati matsango amphesa, Ndi kununkhira kwa mpweya wako ngati maula;