Song of Solomon 8:1 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ha! Achikhala unali mlongo wanga, woyamwa bere limodzi ndi ine! Ndikadakumana nawe panjira, bwenzi ntakumpsompsona, ndipo wina aliyense sakadandinyoza.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mwenzi utakhala ngati mlongo wanga, woyamwa pa bere la amai! Ndikadakupeza panja, ndikadakupsompsona; osandinyoza munthu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ukanakhala kuti ndiwe mlongo wanga, amene anayamwa mawere a amayi anga! Ndikanakumana nawe pa njira, ndikanakupsompsona, ndipo palibe wina aliyense akanandinyoza.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mwenzi utakhala ngati mlongwanga, Woyamwa pa bere la amai! Ndikadakupeza panja, ndikadakupsompsona; Osandinyoza munthu.