Song of Solomon 8:11 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Solomoni anali ndi munda wamphesa ku Baala-Hamoni. Mundawo adaubwereka alimi. Aliyense mwa iwo ankayenera kupereka ndalama zasiliva chikwi chimodzi kuti azilimamo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Solomoni anali ndi munda wamipesa ku Baala-Hamoni; nabwereka alimi mundawo; yense ambwezere ndalama chikwi chifukwa cha zipatso zake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Solomoni anali ndi munda wampesa ku Baala-Hamoni; iyeyo anabwereketsa munda wamphesawo kwa alimi, aliyense mwa iwo ankayenera kupereka ndalama zasiliva 1,000 mʼmalo mwa zipatso zake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Solomo anali ndi munda wamipesa ku Baalahamoni; Nabwereka alimi mundawo; Yense ambwezere ndalama cikwi cifukwa ca zipatso zace.